15 Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israyeli, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala cete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
16 Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; cifukwa cace inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; cifukwa cace iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.
17 Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.
18 Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
19 Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.
20 Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu cakudya ca nsautso, ndi madzi a cipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;
21 ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.