1 Cipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.
2 Lidzaphuka mocuruka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukuru wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukuru wace wa Mulungu wathu.
3 Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.
4 Nenani kwa a mitima ya cinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera cilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.
5 Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.
6 Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba; pakuti m'cipululu madzi adzaturuka, ndi mitsinje m'dziko loti se.
7 Ndipo mcenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.