10 Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.
11 Taona, iwe wamva cimene mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa?
12 Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefi ndi ana a Edeni amene anali m'Telasara.
13 Iri kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamudzi wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iveva?
14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.
15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati,
16 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.