3 Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu, adzachedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu;
4 pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kucokera pakatipo, ndi mzimu wa ciweruziro, ndi mzimu wakutentha.
5 Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ace, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; cifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa cophimba.
6 Ndipo padzakhala cihema ca mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.