23 Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi zonunkhira.
24 Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndarama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi macimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.
25 Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, cifukwa ca Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira macimo ako.
26 Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.
27 Atate wako woyamba anacimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.
28 Cifukwa cace ndidzaipitsa akuru a kacisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israyeli akhale citonzo.