9 Kondwani zolimba, yimbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, waombola Yerusalemu.
10 Yehova wabvula mkono wace woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona cipulumutso ca Mulungu wathu.
11 Cokani inu, cokani inu, turukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; turukani pakati pace, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
12 Pakuti simudzacoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israyeli adzadikira pambuyo panu.
13 Taonani, Mtumiki wanga adzacita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.
14 Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;
15 momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.