1 Iwo amene sanafunsa za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaira andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunachula dzina langa.
2 Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo ao ao;
3 anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;
4 amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;
5 amene ati, Ima pa wekha, usadze cifupi ndi ine, pakuti ine ndiri woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.
6 Taonani, calembedwa pamaso panga; sindidzakhala cete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa cifuwa cao,
7 zoipa zanu zanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandicitira mwano pazitunda; cifukwa cace Ine ndidzayesa nchito yao yakale ilowe pa cifuwa cao.