13 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;
14 taonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wacisoni; ndipo mudzapfuula cifukwa ca kusweka mzimu.
15 Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale citemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzacha atumiki ace dzina lina;
16 comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.
17 Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwa tsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.
18 Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ici ndicilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ace okondwa.
19 Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akupfuula.