4 nukati kwa iye, Cenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, cifukwa ca zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, cifukwa ca mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.
5 Cifukwa Aramu ndi Efraimu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukucitira zoipa, nati,
6 Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timbvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pace, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeeli;
7 atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzacitidwa.
8 Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzatyokatyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;
9 ndipo mutu wa Efraimu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.
10 Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,