1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakuru, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza,
2 Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.
3 Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uche dzina lace, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.
4 Cifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakupfuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, cuma ca Damasiko ndi cofunkha ca Samariya cidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asuri.
5 Ndipo Yehova ananena kwa ine kaciwirinso, nati,
6 Popeza anthu awa akana madzi a Silowa, amene ayenda pang'ono pang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;