7 cifukwa cace, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a Nyanja, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asuri ndi ulemerero wace wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zace zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.
8 Ndipo iye adzapitapitakulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ace, kudzakwanira dziko lanu m'citando mwace, inu Imanueli.
9 Citani phokoso, anthu inu, koma mudzatyokatyoka; cherani khutu, inu nonse a maiko akutari; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka.
10 Panganani upo, koma udzakhala cabe; nenani mau, koma sadzacitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.
11 Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati,
12 Musacinene, Ciwembu; ciri conse cimene anthu awa adzacinena, Ciwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musacite mantha.
13 Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akucititseni mantha Iye.