11 Cifukwa mukondwa, cifukwa musekerera, inu amene mulanda colowa canga, cifukwa muli onenepa monga ng'ombe yamsoti yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;
12 amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, cipululu, dziko louma, bwinja.
13 Cifukwa ca mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babulo adzadabwa, adzatsonyera pa zobvuta zace zonse.
14 Gubani ndi kuzungulira Babulo kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mibvi; pakuti wacimwira Yehova.
15 Mumpfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ace agwa; makoma ace agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; mumbwezere cilango; monga iye wacita mumcitire iye momwemo.
16 Muwathe ofesa ku Babulo, ndi iwo amene agwira zenga nyengo ya masika; cifukwa ca lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ace, nadzathawira yense ku dziko lace.
17 Israyeli ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampitikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asuri; ndipo pomariza Nebukadirezara uyo watyola mafupa ace.