19 Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yace idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.
20 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israyeli, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israyeli, ntheradi.
21 Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.
22 Popeza ngakhale anthu anu Israyeli akunga mcenga wa kunyanja, otsala ao okha okha adzabwera; cionongeko catsimikizidwa, cilungamo cace cisefukira.
23 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu adzacita cionongeko cotsimikizidwa pakati pa dziko lonse lapansi.
24 Cifukwa cace atero Ambuye; Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asuri; ngakhale amenya inu ndi cibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yace, monga amacitira Aigupto.
25 Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.