25 Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.
26 Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira cikoti, monga m'kuphedwa kwa Midyani pa thanthwe la Orebu; ndipo cibonga cace cidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anacitira Aigupto,
27 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wace adzacoka pa phewa lako, ndi gori lace pakhosi pako; ndipo gori lidzathedwa cifukwa ca kudzoza mafuta.
28 Wafika ku Aiati, wapitirira kunka ku Migroni; pa Mikimasi asunga akatundu ace;
29 wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibeya wa Sauli wathawa.
30 Pfuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! tamva, iwe Laisa! iwe Anatoti wosauka!
31 Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhanakutiathawe.