7 Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
8 Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.
9 Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.
10 Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.
11 Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.
12 Yehova, udzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira nchito zathu zonse.
13 Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzachula dzina lanu.