19 Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.
20 Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu cakudya ca nsautso, ndi madzi a cipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;
21 ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
22 Ndipo mudzaipitsa cokuta ca mafano ako, osema asiliva, ndi comata ca mafano ako osungunula agolidi; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Cokani.
23 Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wace adzaca bwino ndi kucuruka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akuru.
24 Momwemonso ng'ombe ndi ana a buru olima nthaka adzadya cakudya cocezera, cimene capetedwa ndi cokokolera ndi mkupizo.
25 Ndipo pamwamba pa mapiri akuru onse, ndipa zitunda zonse zazitaritari padzakhala mitsinje ndi micerenje ya madzi, tsiku lophana lalikuru, pamene nsanja zidzagwa.