2 Ndipo Hezekiya analoza nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,
3 Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndacita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.
4 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,
5 Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.
6 Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.
7 Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;
8 taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.