21 Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; turutsani zifukwa zanu zolimba, ati Mfumu ya Yakobo.
22 Aziturutse, atichulire ife, cimene cidzaoneka; chulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamariziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zirinkudza.
23 Chulani zinthu zimene zirinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, citani zabwino, kapena citani zoipa, kuti ife tiopsyedwe, ndi kuona pamodzi.
24 Taonani, inu muli acabe, ndi nchito yanu yacabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.
25 Ndautsa wina wakucokera kumpoto; ndipo iye wafika wakucokera poturuka dzuwa, amene achula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.
26 Ndani wachula ico ciyambire, kuti ife ticidziwe? ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? inde, palibe wina amene achula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde, palibe wina amene amvetsa mau anu.
27 Poyamba Ine ndidzati kwa Ziyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwa Yerusalemu wina, amene adza ndi mau abwino.