1 Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga.
2 Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.
3 Cifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israyeli, Mpulumutsi wako; ndapatsa Aigupto dombolo lako, Etiopia ndi Seba m'malo mwako.
4 Pokhala iwe wa mtengo wapatari pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.
5 Usaope; pakuti Ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kucokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kucokera kumadzulo.
6 Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi;
7 yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.