13 Cifukwa cace anthu anga amuka m'nsinga, cifukwa ca kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.
14 Ndipo manda akuza cilakolako cace, natsegula kukamwa kwace kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.
15 Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wochuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;
16 koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.
17 Pamenepo ana a nkhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zacilendo zidzadyapo.
18 Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;
19 amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize nchito yace kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israyeli uyandikire, udze kuti tiudziwe!