18 Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;
19 amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize nchito yace kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israyeli uyandikire, udze kuti tiudziwe!
20 Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
21 Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ocenjera!
22 Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali;
23 amene alungamitsa woipa pa cokometsera mlandu, nacotsera wolungama cilungamo cace!
24 Cifukwa cace monga ngati lilime la moto likutha ciputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wobvunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati pfumbi; cifukwa kuti iwo akana cilamulo ca Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israyeli.