8 Pakuti njenjete idzawadya ngati copfunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma cilungamo canga cidzakhala ku nthawi zonse, ndi cipulumutso canga ku mibadwo yonse.
9 Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjiri zipinjiri, amene unapyoza cinjoka cija?
10 Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; amene anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?
11 Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo cisoni ndi kuusa moyo kudzacoka.
12 Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
13 waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse cifukwa ca ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? uli kuti ukali wa wotsendereza?
14 Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posacedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, cakudya cace sicidzasowa.