11 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kaciwiri ndi dzanja lace anthu ace otsala ocokera ku Asuri, ndi ku Aigupto, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja yamcere.
12 Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israyeli, namema obalalika a Yuda, kucokera ku madera anai a dziko lapansi.
13 Ndipo nsanje ya Efraimu idzacoka, ndi iwo amene abvuta Yuda adzadulidwa; Efraimu sacitira nsanje Yuda, ndi Yuda sacitira nsanje Efraimu.
14 Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Moabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.
15 Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Aigupto; ndipo ndi mphepo yace yopsereza adzagwedeza dzanja lace pa Nyanja, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.
16 Ndipo padzakhala khwalala la anthu ace otsala ocokera ku Asuri; monga lija la Israyeli tsiku lokwera iwo kuturuka m'dziko la Aigupto.