1 Khalani cete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni, tiyandikire pamodzi kuciweruziro.
2 Ndani anautsa wina wocokera kum'mawa, amene amuitana m'cilungamo, afike pa phazi lace? Iye apereka amitundu patsogolo pace, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga pfumbi ku lupanga lace, monga ciputu couluzidwa ku uta wace.
3 Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; pa njira imene asanapitemo ndi mapazi ace.
4 Ndani wacipanga, nacimariza ico, kuchula mibadwo ciyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pacimariziro ndine ndemwe.
5 Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.