15 Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? kodi cocekera cidzadzikweza cokha pa iye amene acigwedeza, ngati cibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza iri mtengo.
16 Cifukwa cace Ambuye, Yehova wa makamu, adzarumiza kuonda mwa onenepa ace; ndipo pansi pa ulemerero wace padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.
17 Ndipo kuwala kwa Israyeli kudzakhala moto, ndi Woyera wace adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yace ndi lunguzi wace tsiku limodzi.
18 Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yace, ndi wa m'munda wace wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.
19 Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yace idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.
20 Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israyeli, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israyeli, ntheradi.
21 Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.