17 Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilume lao lilephera, cifukwa ca ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israyeli sindidzawasiya.
18 Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti se, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa cipululu, cikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.
19 Ndidzabzala m'cipululu mkungudza, ndi msangu, ndi mcisu, ndi mtengo waazitona; ndidzaika m'cipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;
20 kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lacita ici, ndipo Woyera wa Israyeli wacilenga ici.
21 Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; turutsani zifukwa zanu zolimba, ati Mfumu ya Yakobo.
22 Aziturutse, atichulire ife, cimene cidzaoneka; chulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamariziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zirinkudza.
23 Chulani zinthu zimene zirinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, citani zabwino, kapena citani zoipa, kuti ife tiopsyedwe, ndi kuona pamodzi.