1 WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,Kapena wosaimirira m'njira ya ocimwa,Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.
2 Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace;Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.
3 Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace,Tsamba lace lomwe losafota;Ndipo zonse azicita apindula nazo.
4 Oipa satero ai;Koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.
5 Cifukwa cace oipa sadzaimirira pa mlanduwo,Kapena ocimwa mu msonkhano wa olungama.
6 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;Koma mayendedwe a oipa adzatayika.