Masalmo 135 BL92

Mulungu alemekezedwa pa ukulu wace. Mafano ndi acabe

1 Haleluya;Lemekezani dzina la Yehova;Lemekezani inu atumiki a Yehova:

2 Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova,M'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

3 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;Muyimbire zolemekeza dzina lace; pakuti nkokondweretsa kutero.

4 Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,Israyeli, akhale cuma cace ceni ceni.

5 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkuru,Ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

6 Ciri conse cimkonda Yehova acicita,Kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

7 Akweza mitambo icokere ku malekezero a dziko lapansi;Ang'animitsa mphezi zidzetse mvula;Aturutsa mphepo mosungira mwace.

8 Anapanda oyamba a Aigupto,Kuyambira munthu kufikira zoweta.

9 Anatumiza zizindikilo ndi zodabwiza pakati pako,Aigupto iwe, Pa Farao ndi pa omtumikira onse.

10 Ndiye amene anapanda amitundu ambiri.Napha mafumu amphamvu;

11 Sihoni mfumu ya Aamori,Ndi Ogi mfumu ya Basana,Ndi maufumu onse a Kanani:

12 Ndipo anapereka dziko lao likhale cosiyira,Cosiyira ca kwa Israyeli anthu ace.

13 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;Cikumbukilo canu, Yehova, kufikira mibadwo mibadwo.

14 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ace,Koma adzaleka atumiki ace.

15 Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golidi,Nchito ya manja a anthu.

16 Pakamwa ali napo koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;

17 Makutu ali nao, koma osamva;Inde, pakamwa pao palibe mpweya.

18 Akuwapanga adzafanana nao;Inde, onse akuwakhulupirira.

19 A nyumba ya Israyeli inu, lemekezani Yehova:A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:

20 A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.

21 Alemekezedwe Yehova kucokera m'Ziyoni,Amene akhala m'Yerusalemu.Haleluya,