Masalmo 45 BL92

Nyimbo voyimbira ukwati wa mfumu

Kwa Mkulu wa Nyimbo pa Syosyanim. Cilangizo ca kwa ana a Kora. Nyimbo ya cikondi.

1 Mtima wanga usefukira naco cinthu cokoma:Ndinena zopeka ine za mfumu:Lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.

2 Inu ndinu wokongola ndithu kuposa ana a anthu;Anakutsanulirani cisomo pa milomo yanu:Cifukwa cace Mulungu anakudalitsani kosatha.

3 Dzimangireni lupanga lanu m'cuuno mwanu, wamphamvu inu,Ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.

4 Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani,Kaamba ka coonadi ndi cifatso ndi cilungamo:Ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.

5 Mibvi yanu njakuthwa;Mitundu ya anthu igwa pansi pa Inu:Iwalasa mumtima adani a mfumu.

6 Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zamkamuyaya:Ndodo yacifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.

7 Mukonda cilungamo, ndipo mudana naco coipa:Cifukwa cace Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inuNdi mafuta a cikondwerero kuposa anzanu.

8 Zobvala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasya;M'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njobvu mwatoruka zoyimba za zingwe zokukondweretsani.

9 Mwa omveka anu muli ana akazi amafumu:Ku dzanja lamanja lanu aima mkazi wa mfumu wobvala golidi wa ku Ofiri.

10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tachera khutu lako;Uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

11 Potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako:Pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.

12 Ndipo mwana wamkazi wa Turo adzafika nayo mphatso;Acuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.

13 Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba:Zobvala zace nza made agolidi.

14 Adzamtsogolera kwa mfumu wabvala zamawanga-mawanga:Anamwali anzace omtsata adzafika nao kwa inu.

15 Adzawatsogolera ndi cimwemwe ndi kusekerera:Adzalowa m'nyumba ya mfumu.

16 M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,Udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.

17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwo mibadwo:Cifukwa cace mitundu ya anthu idzayamika Inu ku nthawi za nthawi.