1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kuca:Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu,M'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,Monga ndinakuonani m'malo oyera.
3 Pakuti cifundo canu ciposa moyo makomedwe ace;Milomo yanga idzakulemekezani.
4 Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;Ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;Ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakupfuula mokondwera;
6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.
7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.
9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.
10 Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;Yense wakulumbirira iye adzatamandira;Pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.