Masalmo 139 BL92

Mulungu ali ponse ponse, adziwa zonse

Kwa Mkulu wa Nsembe. Salmo la Davide.

1 Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.

2 Inumudziwakukhalakwangandi kuuka kwanga,Muzindikira lingaliro langa muli kutali.

3 Muyesa popita ine ndi pogona ine,Ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.

4 Pakuti asanafike mau pa lilime langa,Taonani, Yehova, muwadziwa onse.

5 Munandizinga kumbuyo ndi kumaso,Nimunaika dzanja lanu pa ine.

6 Kudziwa ici kundilaka ndi kundidabwiza:Kundikhalira patali, sindifikirako.

7 Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?

8 Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko;Kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.

9 Ndikadzitengera mapiko a mbanda kuca,Ndi kukhala ku malekezero a nyanja;

10 Kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera,Nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.

11 Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe,Ndi kuunika kondizinga kukhale usiku:

12 Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu,Koma usiku uwala ngati usana:Mdima ukunga kuunika.

13 Pakuti Inu munalenga imso zanga;Munandiumba ndisanabadwe ine.

14 Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe canga ncoopsa ndi codabwiza;Nchito zanu nzodabwiza;Moyo wanga ucidziwa ici bwino ndithu.

15 Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika,Poombedwa ine monga m'munsi mwace mwa dziko lapansi.

16 Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya,Ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu,Masiku akuti ziumbidwe, Pakalibe cimodzi ca izo.

17 Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wace ndithu!Mawerengedwe ace ndi ambirimbiri!

18 Ndikaziwerenga zicuruka koposa mcenga:Ndikauka ndikhalanso nanu.

19 Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu:Ndipo amuna inu nkhumba mwazi, cokani kwa ine.

20 Popeza anena za Inu moipa,Ndi adani anu achula dzina lanu mwacabe.

21 Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova?Ndipo kodi sindimva nao cisoni iwo akuukira Inu?

22 Ndidana nao ndi udani weni weni:Ndiwayesa adani.

23 Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;Mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.

24 Ndipo mupenye ngati ndiri nao mayendedwe oipa,Nimunditsogolere pa njira yosatha.