Masalmo 144 BL92

Davide ayamika Mulungu kuti anamcinjiriza, napempha ampulumutse kuti anthu adalenso

Salmo la Davide.

1 Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,Wakuphunzitsa manja anga acite nkhondo,Zala zanga zigwirane nao:

2 Ndiye cifundo canga, ndi linga langa,Msanje wanga, ndi mpulumutsi wanga;Cikopa canga, ndi Iye amene ndimtama;Amene andigonjetsera anthu anga.

3 Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?Mwana wa munthu kuti mumsamalira?

4 Munthu akunga mpweya;Masiku ace akunga mthunzi wopitirira.

5 Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:Khudzani mapiri ndipo adzafuka.

6 Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa;Tumizani mibvi yanu, ndi kuwapitikitsa,

7 Turutsani manja anu kucokera m'mwamba;Ndikwatuleni ndi kundilanditsa ku madzi akuru,Ku dzanja la alendo;

8 Amene pakamwa pao alankhula zacabe,Ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lacinyengo.

9 Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;Pa cisakasa ca zingwe khumi ndidzayimbira zakukulemekezani.

10 Ndiye amene apatsa mafumu cipulumutso:Amene alanditsa Davide mtumiki wace ku lupanga loipa.

11 Ndilanditseni ndi kundipulumutsa ku dzanja la alendo,Amene pakamwa pao alankhula zacabe,Ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lacinyengo.

12 Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime;Ana athu akazi ngati nsanamira za kungondya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

13 Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundu mitundu;Ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwi zikwi, inde zikwi khumi kubusako.

14 Kuti ng'ombe zathu zikhale zasenza katundu;Ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kuturukamo,Pasakhalenso kupfuula m'makwalala athu.

15 Odala anthu akuona zotere; Odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.