1 Mulungu musakhale cete;Musakhale du, osanena kanthu, Mulungu.
2 Pakuti taonani, adani anu aphokosera:Ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu,
3 Apangana mocenjerera pa anthu anu,Nakhalira upo pa obisika anu.
4 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;Ndipo dzina la Israyeli lisakumbukikenso.
5 Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;Anacita cipangano ca pa Inu:
6 Mahema a Edomu ndi a Aismayeli;Moabu ndi Ahagara;
7 Gebala ndi Amoni ndi Amaleki;Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Turo.
8 Asuri anaphatikana nao;Anakhala dzanja la ana a Loti,
9 Muwacitire monga munacitira Midyani;Ndi Sisera, ndi Jabini ku mtsinje wa Kisoni:
10 Amene anaonongeka ku Endoro;Anakhala ngati ndowe ya kumunda.
11 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;Mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna:
12 Amene anati, TilandeMalo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13 Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;Ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14 Monga moto upsereza nkhalango,Ndi monga lawi liyatsa mapiri;
15 Momwemo muwatsate ndi namondwe,Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.
16 Acititseni manyazi pankhope pao;Kuti afune dzina lanu, Yehova.
17 Acite manyazi, naopsedwe kosatha;Ndipo asokonezeke, naonongeke:
18 Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,Ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.