Masalmo 73 BL92

Kupindula kwa oipa kumakayikitsa pa cilungamo ca Mulungu, koma citsiriziro cao citibvomerezetsa cilungamoco

Salimo la Asafu.

1 Indedi Mulungu acitira Israyeli zabwino,Iwo a mtima wa mbe.

2 Koma ine, ndikadagwa; Mapazi anga akadaterereka,

3 Pakuti ndinacitira nsanje odzitamandira,Pakuona mtendere wa oipa,

4 Pakuti palibe zomangira pakufa iwo:Ndi mphamvu yao niolimba,

5 Sabvutika monga anthu ena;Sasautsika monga anthu ena.

6 Cifukwa cace kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;Acibvala ciwawa ngati malaya.

7 Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao:Malingaliro a mitima yao asefukira.

8 Acita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa:Alankhula modzitama.

9 Pakamwa pao anena zam'mwamba,Ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.

10 Cifukwa cace anthu ace amabwera kudza kuno:Ndipo cikho codzala ndi madzi acigugudiza.

11 Namati, Akacidziwa bwanji Mulungu?Kodi Wam'mwambamwamba ali nayonzeru?

12 Tapenyani, oipa ndi awa;Ndipo pokhazikika cikhazikikire aonjezerapo pa cuma cao.

13 Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwacabe,Ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa;

14 Popeza andisautsa tsiku lonse,Nandilanga mamawa monse,

15 Ndikadati, Ndidzafotokozera cotere,Taonani, ndikadacita cosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.

16 Pamene ndinayesa kudziwitsa ici,Ndinabvutika naco;

17 Mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu,Ndi kulingalira citsiriziro cao.

18 Indedi muwaika poterera:Muwagwetsa kuti muwaononge.

19 Ha! m'kamphindi ayesedwa bwinja;Athedwa konse ndi zoopsya.

20 Monga anthu atauka, apepula loto;Momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa cithunzithunzi cao.

21 Pakuti mtima wanga udawawa,Ndipo ndinalaswa m'imso zanga;

22 Ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu;Ndinali ngati nyama pamaso panu.

23 Koma ndikhala ndi Inu cikhalire:Mwandigwira dzanja langa la manja.

24 Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu,Ndipo mutatero, mudzandilandira m'ulemerero,

25 Ndiri ndi yani Kumwamba, koma Inu?Ndipo Pa dziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.

26 Likatha thupi langa ndi mtima wanga:Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi colandira canga cosatha.

27 Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka;Muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

28 Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu:Ndimuyesa Ambuye Yehova pathawirapo ine,Kuti ndifotokozere nchito zanu zonse,