Masalmo 145 BL92

Ukuru ndi ukoma wa Mulungu

Salmo lolemekeza; la Davide,

1 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

2 Masiku onse ndidzakuyamikani;Ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

3 Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukuru;Ndi ukulu wace ngwosasanthulika.

4 Mbadwo wina udzalemekezera nchito zanu mbadwo unzace,Ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

5 Ndidzalingalira ulemerero waukuru wa ulemu wanu,Ndi nchito zanu zodabwiza.

6 Ndipo adzanenera mphamvu za nchito zanu zoopsa;Ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7 Adzabukitsa cikumbukilo ca ubwino wanu waukuru,Nadzayimbira cilungamo canu.

8 Yehova ndiye wacisomo, ndi wacifundo;Osakwiya msanga, ndi wa cifundo cacikuru.

9 Yehova acitira cokoma onse;Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.

10 Nchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;Ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11 Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,Adzalankhulira mphamvu yanu;

12 Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zace,Ndi ulemerero waukuru wa ufumu wace.

13 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,Ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.

14 Yehova agwiriziza onse akugwa,Naongoletsa onse owerama.

15 Maso a onse ayembekeza Inu;Ndipo muwapatsa cakudya cao m'nyengo zao.

16 Muniowetsa dzanja lanu,Nimukwaniritsira zamoyo zonse cokhumba cao.

17 Yehova ali wolungama m'njira zace zonse,Ndi wacifundo m'nchito zace zonse.

18 Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,Onse akuitanira kwa Iye m'coonadi.

19 Adzacita cokhumba iwo akumuopa;Nadzamva kupfuula kwao, nadzawapulumutsa.

20 Yehova asunga onse akukondana naye;Koma oipa onse adzawaononga.

21 Pakamwa panga padzanena cilemekezo ca Yehova;Ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lace loyera ku nthawi za nthawi.