1 Iwo akukhulupirira YehovaAkunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha,
2 Monga mapiri azinga Yerusalemu,Momwemo Yehova azinga anthu ace,Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
3 Pakuti ndodo yacifumu ya coipa siidzapumula pa gawo la olungama;Kuti olungama asaturutse dzanja lao kucita cosalungama,
4 Citirani cokoma, Yehova, iwo okhala okoma;Iwo okhala oongoka mumtima mwao.
5 Koma iwo akupatuka kutsata njira zao zokhotakhota,Yehova adzawacotsa pamodzi ndi ocita zopanda pace.Mtendere ukhale pa Israyeli.