Masalmo 10 BL92

Athamangira Mulungu pothawa adani omtsata

1 Muimiranji patari, Yehova?Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;Agwe m'ciwembu anapanganaco.

3 Pakuti woipa adzitamira cifuniro ca moyo wace,Adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

4 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yace, akuti, Sadzafunsira.Malingaliro ace onse akuti, Palibe Mulungu.

5 Mayendedwe ace alimbika nthawi zonse;Maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;Adani ace onse awanyodola.

6 Ati mumtima mwace, Sindidzagwedezeka ine;Ku mibadwo mibadwo osagwa m'tsoka ine.

7 M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera;Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.

8 Akhala m'molalira midzi;Mobisalamo akupha munthu wosacimwa:Ambisira waumphawi nkhope yace,

9 Alalira monga mkango m'ngaka mwace;Alalira kugwira wozunzika:Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace.

10 Aunthama, nawerama,Ndipo aumphawi agwa m'zala zace.

11 Anena m'mtima mwace, Mulungu waiwala;Wabisa nkhope yace; sapenya nthawi zonse,

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;Musaiwale ozunzika.

13 Woipa anyozeranii Mulungu,Anena m'mtima mwace, Simudzafunsira?

14 Mwapenya; pakuti mumayang'anira cibvutitso ndi cisoni kuti acipereke m'manja mwanu;Waumphawi adzipereka kwa Inu;Wamasiye mumakhala mthandizi wace.

15 Thyolani mkono wa woipa;Ndipo wocimwa, mutsate coipa cace kufikira simucipezanso cina.

16 Yehova ndiye Mfumu ku nthawi yamuyaya;Aonongeka amitundu m'dziko lace.

17 Yehova, mwamva cikhumbo ca ozunzika:Mudzakhazikitsa mtima wao, mudzachereza khutu lanu:

18 Kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,Kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa.