Masalmo 104 BL92

Ulemerero wa Mulungu m'zolengedwa ndi m'kuzisunga komwe

1 Lemekeza Yehova, moyo wanga;Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkurukuru;

2 Mubvala ulemu ndi cifumu.Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi cobvala;Ndi kuyala thambo ngati nsaru yocinga;

3 Amene alumikiza mitanda ya zipinda zace m'madzi;Naika makongwa akhale agareta ace;Nayenda pa mapiko a mphepo;

4 Amene ayesa mphepo amithenga ace;Lawi la moto atumiki ace;

5 Anakhazika dziko lapansi pa maziko ace,Silidzagwedezeka ku nthawi yonse.

6 Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi cobvala;Madzi anafikira pamwamba pa mapiri,

7 Pa kudzudzula kwanu anathawa;Anathawa msanga liu la bingu lanu;

8 Anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa,Kufikira malo mudawakonzeratu.

9 Munaika malire kuti asapitirireko;Kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

10 Atumiza akasupe alowe m'makwawa;Ayenda pakati pa mapiri:

11 Zimamwamo nyama zonse za kuthengo;Mbidzi zipherako ludzu lao.

12 Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo,Zimayimba pakati pa mitawi.

13 Iye amwetsa mapiri mocokera m'zipinda zace:Dziko lakhuta zipatso za nchito zanu.

14 Ameretsa msipu ziudye ng'ombe,Ndi zitsamba acite nazo munthu;Naturutse cakudya cocokera m'nthaka;

15 Ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,Ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yace,Ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

16 Mitengo ya Mulungu yadzala ndi madzi;Mikungudza ya ku Lebano imene anaioka;

17 M'mwemo mbalame zimanga zisa zao;Pokhala cumba mpa mitengo ya mikungudza,

18 Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma;Pamatanthwe mpothawirapo mbira.

19 Anaika mwezi nyengo zace;Dzuwa lidziwa polowera pace.

20 Muika mdima ndipo pali usiku;Pamenepo zituruka zirombo zonse za m'thengo.

21 Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao,Nifuna cakudya cao kwa Mulungu.

22 Poturuka dzuwa, zithawa, Zigona pansi m'ngaka mwao.

23 Pamenepo munthu aturukira ku nchito yace,Nagwiritsa kufikira madzulo.

24 Nchito zanu zicurukadi, Yehova!Munazicita zonse mwanzeru;Dziko lapansi lidzala naco cuma canu.

25 Nyanja siyo, yaikuru ndi yacitando,M'mwemo muli zokwawa zosawerengeka;Zamoyo zazing'ono ndi zazikuru.

26 M'mwemo muyenda zombo;Ndi livyatanu amene munamlenga aseweremo.

27 Izi zonse zikulindirirani,Muzipatse cakudya cao pa nyengo yace.

28 Cimene muzipatsa zigwira;Mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.

29 Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa;Mukalanda mpweya wao, zikufa,Nizibwerera kupfumbi kwao.

30 Potumizira mzimu wanu, zilengedwa;Ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.

31 Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha;Yehova akondwere mu nchito zace;

32 Amene apenyerera pa dziko lapansi, ndipo linjenjemera;Akhudza mapiri, ndipo afuka.

33 Ndidzayimbira Yehova m'moyo mwanga:Ndidzayimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndiripo.

34 Pomlingirira Iye pandikonde;Ndidzakondwera mwa Yehova.

35 Ocimwa athedwe ku dziko lapansi,Ndi oipa asakhalenso.Yamika Yehova, moyo wanga.Haleluya.