1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu!
2 Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace,Ndipo simunakana pempho la milomo yace.
3 Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma:Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace.
4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi.
5 Ulemerero wace ngwaukuru mwa cipulumutso canu:Mumcitira iye ulemu ndi ukulu.
6 Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.
7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,Ndipo mwa cifundo ca Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye,
8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse:Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.
9 Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.Yehova adzawatha m'kukwiya kwace,Ndipo moto udzawanyeketsa.
10 Mudzaziononga zobala zao kuzicotsa pa dziko lapansi,Ndi mbeu zao mwa ana a anthu.
11 Pakuti anakupangirani coipa:Anapangana ciwembu, osakhoza kucicita.
12 Pakuti mudzawabweza m'mbuyo,Popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao,
13 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu:Potero tidzayimba ndi kulemekeza cilimbiko canu.