Masalmo 109 BL92

Davide apempha Mulungu alange oipa, amlanditse m'manja mwao

Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salmo la Davide,

1 Mulungu wa cilemekezo canga, musakhale cete;

2 Pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa cinyengo pananditsegukira;Anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.

3 Ndipo anandizinga ndi mau a udani,Nalimbana nane kopanda cifukwa.

4 M'malo mwa cikondi canga andibwezera udani;Koma ine, kupemphera ndiko.

5 Ndipo anandisenza coipa m'malo mwa cokoma,Ndi udani m'malo mwa cikondi canga.

6 Muike munthu woipa akhale mkuru wace;Ndi mdani aime pa dzanja lamanja lace.

7 Ponenedwa mlandu wace aturuke wotsutsika;Ndi pemphero lace likhale ngati kucimwa.

8 Masiku ace akhale owerengeka;Wina alandire udindo wace.

9 Ana ace akhale amasiye, Ndi mkazi wace wamasiye.

10 Ana ace akhale amcirakuyenda ndi opemphapempha;Afunefune zosowa zao kucokera m'mabwinja mwao.

11 Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;Ndi alendo alande za nchito yace.

12 Pasakhale munthu wakumdtira cifundo;Kapena kucitira cokoma ana ace amasiye.

13 Zidzukulu zace zidulidwe;Dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.

14 Mphulupulu za makolo ace zikumbukike ndi Yehova;Ndi cimo la mai wace lisafafanizidwe.

15 Zikhale pamaso pa Yehova cikhalire,Kuti adule cikumbukilo cao kucicotsera ku dziko lapansi.

16 Cifukwa kuti sanakumbukila kucita cifundo,Koma analondola wozunzika ndi waumphawi,Ndi wosweka mtima, kuti awaphe.

17 Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini;Sanakondwera nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.

18 Anabvalanso temberero ngati maraya,Ndipo lidamlowa m'kati mwace ngati madzi,Ndi ngati mafuta m'mafupa ace.

19 Limkhalire ngati cobvala adzikuta naco,Ndi lamba limene adzimangirira nalo m'cuuno cimangirire,

20 Ici cikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova,Ndi ya iwo akunenera coipa moyo wanga.

21 Koma Inu, Yehova Ambuye, mucite nane cifukwa ca dzina lanu;Ndilanditseni popeza cifundo canu ndi cabwino.

22 Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi,Ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga.

23 Ndamuka ngati mthunzi womka m'taliNdiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.

24 Mabondo anga agwedezeka cifukwa ca kusala;Ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.

25 Ndiwakhaliranso cotonza;Pakundiona apukusa mutu.

26 Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga:Ndipulumutseni monga mwa cifundo canu;

27 Kuti adziwe kuti ici ndi dzanja lanu;Kuti Inu Yehova munacicita.

28 Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu;Pakuuka iwowa adzacita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.

29 Otsutsana nane abvale manyazi,Nadzikute naco cisokonezo cao ngati ndi copfunda.

30 Ndidzayamika Yehova kwakukuru pakamwa panga;Ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.

31 Popeza adzaima pa dzanja lamanja la waumphawiKumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wace.