1 Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda cifundo:Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?Ndimayenderanji woliralira cifukwa ca kundipsinja mdani?
3 Tumizirani kuunika kwanu ndi coonadi canu zinditsogolere:Zindifikitse ku phiri lanu loyera,Kumene mukhala Inuko.
4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,Kufikira Mulungu wa cimwemwe canga ceniceni:Ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.