Masalmo 105 BL92

Alemekeza Yehova pa zodabwiza adazicitira ana a Israyeli

1 Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita Iye.

2 Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.

3 Mudzitamandire ndi dzina lace loyera:Mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.

4 Funani Yehova, ndi mphamvu yace;Funsirani nkhope yace nthawi zonse.

5 Kumbukilani zodabwiza zace adazicita;Zizindikilo zace ndi maweruzo a pakamwa pace;

6 Inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.

7 Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi.

8 Akumbukila cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

9 Cipanganoco anapangana ndi Abrahamu,Ndi lumbiro lace ndi Isake;

10 Ndipo anaciimikira Yakobo, cikhale malemba,Cikhale cipangano cosatha kwa Israyeli.

11 Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,Gawo la colandira cako;

12 Pokhala iwo anthu owerengeka,Inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;

13 Nayendayenda kucokera mtundu wina kufikira mtundu wina,Kucokera ufumu wina kufikira anthu ena.

14 Sanalola munthu awasautse;Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa;

15 Ndi kuti musamakhudza odzozedwa anga,Musamacitira coipa aneneri anga.

16 Ndipo anaitana njala igwere dziko;Anatyola mcirikizo wonse wa mkate.

17 Anawatsogozeratu munthu;Anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:

18 Anapweteka miyendo yace ndi matangadza;Anamgoneka m'unyolo;

19 Kufikira nyengo yakucitika maneno ace;Mau a Yehova anamuyesa.

20 Mfumuyo anatuma munthu nammasula;Woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.

21 Anamuika akhale woyang'anira nyumba yace,Ndi woweruza wa pa zace zonse:

22 Amange nduna zace iye mwini,Alangize akulu ace adziwe nzeru.

23 Pamenepo Israyeli analowa m'Aigupto;Ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.

24 Ndipo anacurukitsatu mtundu wa anthu ace,Nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.

25 Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ace,Kuti acite monyenga ndi atumiki ace.

26 Anatuma Mose mtumiki wace, Ndi Aroni amene adamsankha.

27 Anaika pakati pao zizindikilo zace,Ndi zodabwiza m'dziko la Hamu.

28 Anatumiza mdima ndipo kunada;Ndipo sanapikisana nao mau ace.

29 Anasanduliza madzi ao akhale mwazi,Naphanso nsomba zao.

30 Dziko lao linacuruka acule,M'zipinda zomwe za mafumu ao.

31 Ananena, ndipo inadza mitambo ya nchenche,Ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.

32 Anawapatsa mvula yamatalala,Lawi la moto m'dziko lao.

33 Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao;Natyola mitengo kufikira m'malire ao onse.

34 Ananena, ndipo linadza dzombeNdi mphuci, ndizo zosawerengeka,

35 Ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao,Zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.

36 Ndipo Iye anapha acisamba onse m'dziko mwaoCoyambira ca mphamvu yao yonse.

37 Ndipo anawaturutsa pamodzi ndi siliva ndi golidi:Ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.

38 Aigupto anakondwera pakucoka iwo;Popeza kuopsa kwao kudawagwera.

39 Anayala mtambo uwaphimbe;Ndi moto uunikire usiku,

40 Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri.Nawakhuritsa mkate wakumwamba.

41 Anatsegula pathanthwe, anaturukamo madzi;Nayenda pouma ngati mtsinje.

42 Popeza anakumbukila mau ace oyera,Ndi Abrahamu mtumiki wace.

43 Potero anaturutsa anthu ace ndi kusekerera,Osankhika ace ndi kupfuula mokondwera.

44 Ndipo anawapatsa maiko a amitundu;Iwo ndipo analanda zipatso za nchito ya anthu:

45 Kuti asamalire malemba ace,Nasunge malamulo ace.Haleluya.