Masalmo 86 BL92

Davide apempha Mulungu kolimba amlanditse

Pemphero la Davide.

1 Cherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.

2 Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.

3 Mundicitire cifundo, Ambuye;Pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.

4 Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;Pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.

5 Pakuti fnu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,Ndi wa cifundo cocurukira onse akuitana Inu.

6 Cherani khutu pemphero langa, Yehova;Nimumvere mau a kupemba kwanga,

7 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;Popeza mudzandibvomereza.

8 Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;Ndipo palibe nchito zonga zanu.

9 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; Nadzalemekeza dzina lanu.

10 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakucita zodabwiza;Inu ndinu Mulungu, nokhanu.

11 Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'coonadi canu:Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

12 Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.

13 Pakuti cifundo canu ca pa ine ncacikuru;Ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

14 Mulungu, odzikuza andiukira,Ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,Ndipo sanaika Inu pamaso pao.

15 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo,Wosapsa mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.

16 Mundibwerere ine, ndi kundicitira cifundo;Mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,Ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.

17 Mundicitire cizindikilo coti cabwino;Kuti ondida acione, nacite manyazi,Popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa,