Masalmo 42 BL92

Mtima wolira kuyanjana ndi Mulungu m'Kacisi

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Cilangizo ca kwa ana a Kora.

1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;Motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo:Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?

3 Misozi yanga yakhalangati cakudya canga,Usana ndi usiku;Pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?

4 Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine,Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu,Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika,Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikansoCifukwa ca cipulumutso ca nkhope yace.

6 Mulungu wanga, moyo wangaUdziweramira m'kati mwanga;Cifukwa cace ndikumbukila Inu m'dziko la Yordano,Ndi mu Ahermone, m'kaphiri ka Mizara.

7 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,Pa mkokomo wa matiti anu: Mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.

8 Koma usana Yehova adzalamulira cifundo cace,Ndipo usiku Nyimbo yace idzakhala ndi ine.Inde pemphero la kwa Yehova wa moyowanga.

9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala cifukwa ninji?Ndimayenderanji wakulira Cifukwa ca kundipsinja mdaniyo?

10 Adani anga andinyoza ndi kundityola mafupa anga;Pakunena ndine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?

11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga ndi Mulungu wanga,