Masalmo 106 BL92

Israyeli anapikisana ndi Yehova kwambiri, Iye nawalanga nawalanditsanso Amlemekezepo

1 Haleluya.Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino:Pakuti cifundo cace ncosatha.

2 Adzafotokoza ndani nchito zamphamvu za Yehova,Adzamveketsa ndani cilemekezo cace conse?

3 Odala iwo amene asunga ciweruzo,Iye amene acita cilungamo nthawi zonse.

4 Mundikumbukile, Yehova, monga momwe mubvomerezana ndi anthu anu;Mundionetsa cipulumutso canu:

5 Kuti ndione cokomaco ca osankhika anu,Kuti ndikondwere naco cikondwerero ca anthu anu,Kuti ndidzitamandire pamodzi ndi colowa canu.

6 Talakwa pamodzi ndi makolo athu;Tacita mphulupulu, tacita coipa.

7 Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto;Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji;Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.

8 Koma anawapulumutsa cifukwa ca dzina lace,Kuti adziwitse cimphamvu cace.

9 Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa:Potero anawayendetsa mozama ngati m'cipululu.

10 Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada,Nawaombola ku dzanja la mdani.

11 Ndipo madziwo anamiza owasautsa;Sanatsala mmodzi yense.

12 Pamenepo anabvomereza mau ace;Anayimbira comlemekeza.

13 Koma anaiwala nchito zace msanga;Sanalindira uphungu wace:

14 Popeza analaka-lakatu kucidikhako,Nayesa Mulungu m'cipululu.

15 Ndipo anawapatsa copempha iwo;Koma anaondetsa mitima yao.

16 Ndipo kumisasa anacita nao nsanje MoseNdi Aroni woyerayo wa Yehova.

17 Dziko lidayasama nilidameza Datani,Ndipo linafotsera gulu la Abiramu.

18 Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto;Lawi lace lidapsereza oipawo.

19 Anapanga mwana wa ng'ombe ku Horebu,Nagwadira fano loyenga.

20 M'mwemo anasintha ulemerero waoNdi fanizo la ng'ombe Yakudya msipu.

21 Anaiwala Mulungu mpulumutsi wao,Amene anacita zazikulu m'Aigupto;

22 Zodabwiza m'dziko la Hamu,Zoopsa ku Nyanja Yofiira.

23 Potero Iye adati awaononge,Pakadapanda Mose wosankhika wace, kuima pamaso pace pagamukapo,Kubweza ukali wace ungawaononge,

24 Anapeputsanso dziko lofunika,Osabvomereza mau ace;

25 Koma anadandaula m'mahema mwao,Osamvera mau a Yehova.

26 Potero anawasamulira dzanja lace,Kuti awagwetse m'cipululu:

27 Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu,Ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.

28 Ndipo anadzipatikiza ndi BaalaPeori,Nadyanso nsembe za akufa.

29 Ndipo anamkwiyitsa nazo zocita zao;Kotero kuti mliri unawagwera.

30 Pamenepo panauka Pinehasi, nacita cilango:Ndi mliriwo unaletseka.

31 Ndipo adamuyesa iye wacilungamo,Ku mibadwo mibadwo ku nthawi zonse.

32 Anautsanso mkwiyo wace ku madzi a Meriba,Ndipo kudaipira Mose cifukwa ca iwowa:

33 Pakuti anawawitsa mzimu wace,Ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yace.

34 Sanaononga mitunduyo ya anthu,Imene Mulungu adawauza;

35 Koma anasokonekerana nao amitundu,Naphunzira nchito zao:

36 Ndipo anatumikira mafano ao,Amene anawakhalira msampha:

37 Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda,

38 Nakhetsa mwazi wosacimwa, ndi wo mwazi wa ana ao amuna ndi akazi,Amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani;M'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

39 Ndipo anadziipsa nazo nchito zao,Nacita cigololo nao macitidwe ao.

40 Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ace,Nanyansidwa Iye ndi colowa cace.

41 Ndipo anawapereka m'manja a amitundu;Ndipo odana nao anacita ufumu pa iwo.

42 Adani ao anawasautsanso,Nawagonjetsa agwire mwendo wao.

43 Iye anawalanditsa kawiri kawiri;Koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao,Ndi mphulupulu zao zinawafoketsa,

44 Koma anapenya nsautso yao,Pakumva kupfuula kwao:

45 Ndipo anawakumbukila cipangano cace,Naleza monga mwa kucuruka kwa cifundo cace.

46 Ndipo anawacitira kuti apeze nsoniPamaso pa onse amene adawamanga ndende.

47 Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu,Ndi kutisokolotsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.

48 Wodala Yehova, Mulungu wa Israyeli,Kuyambira kosayamba kufikira kosatha.Ndi anthu onse anene, Amen.Haleluya,