Masalmo 78 BL92

Cikondi ndi cipiriro ca'Mulungu ca pa Aisrayeli osakhulupirika

Cilangizo ca Asatu.

1 Tamverani, anthu anga, cilamulo canga;Cherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.

2 Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira;Ndidzachula zinsinsi zoyambira kale;

3 Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa,Ndipo makolo athu anatifotokozera.

4 Sitidzazibisira ana ao,Koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova,Ndi mphamvu yace, ndi zodabwiza zace zimene anazicita.

5 Anakhazika mboni mwa Yakobo,Naika cilamulo mwa Israyeli,Ndizo analamulira atate athu,Akazidziwitse ana ao;

6 Kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa;Amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao:

7 Ndi kuti ciyembekezo cao cikhale kwa Mulungu,Osaiwala zocita Mulungu,Koma kusunga malamulo ace ndiko.

8 Ndi kuti asange makolo ao,Ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu;Mbadwo wosakonza mtima wao,Ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.

9 Ana a Efraimu okhala nazo zida, oponya nao mauta,Anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo.

10 Sanasunga cipangano ca Mulungu,Nakana kuyenda m'cilamulo cace.

11 Ndipo anaiwala zocita Iye,Ndi zodabwiza zace zimene anawaonetsa.

12 Anacita codabwiza pamaso pa makolo ao,M'dziko la Aigupto ku cidikha ca Zoanu.

13 Anagawa nyanja nawapititsapo;Naimitsa madziwo ngati khoma.

14 Ndipo msana anawatsogolera ndi mtamboNdi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.

15 Anang'alula thanthwe m'cipululu,Ndipo anawamwetsa kocuruka monga m'madzi ozama.

16 Anaturukitsa mitsinje m'thanthwe,Inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje.

17 Koma anaonjeza kuincimwira Iye,Kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'cipululu.

18 Ndipo anayesa Mulungu mumtimamwaoNdi kupempha cakudya monga mwa kulakalaka kwao.

19 Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;Anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'cipululu?

20 Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendakoNdi mitsinje inasefuka;Kodi adzakhozanso kupatsa mkate?Kodi adzafunira anthu ace nyama?

21 Cifukwa cace Yehova anamva, nakwiya;Ndipo anayatsa moto pa Yakobo,Ndiponso mkwiyo unakwera pa Israyeli;

22 Popeza sanakhulupirira Mulungu,Osatama cipulumutso cace.

23 Koma analamulira mitambo iri m'mwamba,Natsegula m'makomo a kumwamba.

24 Ndipo anawabvumbitsira mana, adye,Nawapatsa tirigu wa kumwamba.

25 Yense anadya mkate wa omveka:Anawatumizira cakudya cofikira,

26 Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa:Natsogoza mwela ndi mphamvu yace.

27 Ndipo anawabvumbitsira nyama ngati pfumbi,Ndi mbalame zouluka ngati mcenga wa kunyanja:

28 Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao,Pozungulira pokhala iwo.

29 Potero anadya nakhuta kwambiri;Ndipo anawapatsa cokhumba iwo.

30 Asanathe naco cokhumba cao,Cakudya cao ciri m'kamwa mwao,

31 Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira,Ndipo anapha mwa onenepa ao,Nagwetsa osankhika a Israyeli.

32 Cingakhale ici conse anacimwanso,Osabvomereza zodabwiza zace.

33 Potero anathera masiku ao ndi zopanda pace,Ndi zaka zao mwa mantha.

34 Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye;Nabwerera, nafunitsitsa Mulungu,

35 Ndipo anakumbukila kuti Mulungu ndiye thanthwe lao,Ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao.

36 Koma anamsyasyalika pakamwa pao,Namnamiza ndi lilime lao.

37 Popeza mtima wao sunakonzekera Iye,Ndipo sanakhazikika m'cipangano cace.

38 Koma Iye pokhala ngwa cifundo,Anakhululukira coipa, osawaononga;Nabweza mkwiyo wace kawiri kawiri,Sanautsa ukali wace wonse.

39 Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu;Mphepo yopita yosabweranso.

40 Kawiri kawiri nanga anapikisana ndi Iye kucigwako,Nammvetsa cisoni m'cipululu.

41 Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu,Nacepsa Woyerayo wa Israyeli.

42 Sanakumbukila dzanja lace,Tsikuli anawaombola kwa msautsi.

43 Amene anaika zizindikilo zace m'Aigupto,Ndi zodabwiza zace ku cidikha ca Zoanu;

44 Nasanduliza nyanja yao mwazi,Ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.

45 Anawatumizira pakati pao mitambo ya nchenche zakuwatha;Ndi acule akuwaononga.

46 Ndipo anapatsa mphuci dzinthu dzao,Ndi dzombe nchito yao.

47 Anapha mphesa zao ndi matalala,Ndi mikuyu yao ndi cisanu.

48 Naperekanso zoweta zao kwa matalala,Ndi ng'ombe zao kwa mphezi.

49 Anawatumizira mkwiyo wace wotentha,Kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso,Ndizo gulu la amithenga ocita zoipa.

50 Analambulira mkwiyo wace njira;Sanalekerera moyo wao usafe,Koma anapereka moyo wao kumliri;

51 Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Aigupto,Ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu:

52 Koma anaturutsa anthu ace ngati nkhosa,Nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'cipululu.

53 Ndipo anawatsogolera mokhulupirika,Kotero kuti sanaopa;Koma nyanja inamiza adani ao.

54 Ndipo anawafikitsa ku malire a malo ace oyera,Ku phiri ili, dzanja lamanja lace lidaligula.

55 Ndipo anapitikitsa amitundu pamaso pao,Nawagawira colowa cao, ndi muyeso,Nakhalitsa mafuko a Israyeli m'mahema mwao.

56 Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba,Osasunga mboni zace;

57 Koma anabwerera m'mbuyo, nacita zosakhulupirika monga makolo ao:Anapatuka ngati uta wolenda,

58 Ndipo anautsa mtima wace ndi malo amsanje ao,Namcititsa nsanje ndi mafano osema.

59 Pakumva ici Mulungu, anakwiya, Nanyozatu Israyeli;

60 Ndipo anacokera cokhalamo ca ku Silo,Cihemaco adacimanga mwa anthu;

61 Napereka mphamvu yace m'ukapolo,Ndi ulemerero wace m'dzanja la msautsi.

62 Naperekanso anthu ace kwa lupanga;Nakwiya naco colandira cace.

63 Moto unapsereza anyamata ao;Ndi anamwali ao sanalemekezeka.

64 Ansembe ao anagwa ndi lupanga;Ndipo amasiye ao sanacita maliro.

65 Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo;Ngati ciphona cakucita nthungululu ndi vinyo.

66 Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo;Nawapereka akhale otonzeka kosatha.

67 Tero anakana hema wa Yosefe;Ndipo sanasankha pfuko la Efraimu;

68 Koma anasankha pfuko la Yuda,Phiri la Ziyoni limene analikonda.

69 Ndipo anamanga malo oyera ace ngati kaphiri,Monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.

70 Ndipo anasankha Davide mtumiki wace,Namtenga ku makola a nkhosa:

71 Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa,Awete Yakobo, anthu ace, ndi Israyeli, colandira cace.

72 Potero anawaweta monga mwa mtima wace wangwiro;Nawatsogolera ndi luso la manja ace.