Masalmo 22 BL92

Posautsidwa Davide adandaulira, apemphera, ayamika Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Ajelet Hasakara, Salmo la Davide.

1 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?Mukhaliranji kutali kwa cipulumutso canga, ndi kwa mau a kubuula kwanga?

2 Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simubvomereza;Ndipo usiku, sindikhala cete.

3 Koma Inu ndinu woyera,Wakukhala m'malemekezo a Israyeli.

4 Makolo athu anakhulupirira Inu:Anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.

5 Anapfuula kwa Inu, napulumutsidwa:Anakhulupita Inu, ndipo sanacita manyazi.

6 Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai:Cotonza ca anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.

7 Onse akundipenya andiseka:Akwenzula, apukusa mutu, nati,

8 Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,Amlanditse tsopano popeza akondwera naye.

9 Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa:Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.

10 Cibadwire ine anandisiyira Inu:Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.

11 Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi:Pakuti palibe mthandizi.

12 Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga:Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,

13 Andiyasamira m'kamwa mwao,Ngati mkango wozomola ndi wobangula.

14 Ndathiridwa pansi monga madzi,Ndipo mafupa anga onse anaguluka:Mtima wanga ukunga sera; Wasungunuka m'kati mwa matumbo anga,

15 Mphamvu yanga yauma ngati phale;Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga;Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.

16 Pakuti andizinga agaru:Msonkhano wa oipa wanditsekereza;Andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.

17 Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse;Iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine:

18 Agawana zobvala zanga,Nalota maere pa malaya anga,

19 Koma Inu, Yehova, musakhale kutari;Mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.

20 Landitsani moyo wanga kulupanga;Wokondedwa wanga ku mphamvu ya garu,

21 Ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango;Inde mwandiyankha ine ndiri pa nyanga za njati,

22 Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga:Pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.

23 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;Inu nonse mbumba ya Yakobo, mumcitire ulemu;Ndipo mucite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israyeli.

24 Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika;Ndipo sanambisira nkhope yace;Koma pompfuulira Iye, anamva.

25 Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukuru:Zowinda zanga ndidzazicita pamaso pa iwo akumuopa Iye.

26 Ozunzika adzadya nadzakhuta:Adzayamika Yehova iwo amene amfuna:Ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.

27 Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukila nadzatembenukira kwa Yehova:Ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.

28 Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;Iye acita ufumu mwa amitundu.

29 Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira:Onse akutsikira kupfumbi adzawerama pamaso pace,Ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wace.

30 Mbumba ya anthu idzamtumikira;Kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.

31 Iwo adzadza nadzafotokozera cilungamo caceKwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anacicita.