Masalmo 74 BL92

Malo oyera adetsedwa. Apempha Mulungu akumbuke cipangano cao

Cilangizo ca Asaru.

1 Mulungu, munatitayiranji citayire?Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

2 Kumbukilani msonkhano wanu, umene munaugula kale,Umene munauombola ukhale pfuko la colandira canu;Phiri La Ziyoni limene mukhalamo.

3 Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,Zoipa zonse adazicita mdani m'malo opatulika.

4 Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;Aika mbendera zao zikhale zizindikilo.

5 Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.

6 Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zace zonseNdi nkhwangwa ndi nyundo,

7 Anatentha malo anu opatulika;Anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.

8 Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;Anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.

9 Sitiziona zizindikilo zathu;Palibenso mneneri;Ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.

10 Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

11 Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?Muliturutse ku cifuwa canu ndipo muwatheretu.

12 Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,Wocita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi.

13 Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu;Mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi.

14 Mudaphwanya mitu ya livyatanu;Mudampereka akhale cakudya ca iwo a m'cipululu.

15 Mudagawa kasupe ndi mtsinje;Mudaphwetsa mitsinje yaikuru.

16 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu:Munakonza kuunika ndi dzuwa.

17 Munaika malekezero onse a dziko lapansi;Munalenga dzinja ndi malimwe.

18 Mukumbukile ici, Yehova, mdaniyo anatonza,Ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa cirombo;Musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.

20 Samalirani cipanganoco;Pakuti malo amdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo ciwawa.

21 Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;Wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.

22 Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha;Kumbukilani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.

23 Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu;Kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakweca kosaleka.