Masalmo 77 BL92

Acitankhawapokumbuka zocita Mulungu, koma alimbika mtima pokumbuka zina adazicita Iye

Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yedutunu; Salmo la Asaru.

1 Ndidzapfuulira kwa Mulungu ndi mau anga;Kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzandicherezera khutu.

2 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye:Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka;Mtima wanga unakanakutonthozedwa.

3 Ndikumbukila Mulungu ndipo ndibvutika;Ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.

4 Mundikhalitsa maso;Ndigwidwa mtima wosanena kanthu.

5 Ndinaganizira masiku akale, zaka zakalekale.

6 Ndikumbukila Nyimbo yanga, usiku;Ndilingalira mumtima mwanga;Mzimu wanga unasanthula.

7 Kodi Mulungu adzataya nthawi yonse?Osabwerezanso kukondwera nafe.

8 Cifundo cace calekeka konse konse kodi?Lonjezano lace lidatha kodi ku mibadwo yonse?

9 Kodi Mulungu waiwala kucita cifundo?Watsekereza kodi nsoni zokoma zace mumkwiyo?

10 Ndipo ndinati, Cindilaka ici;Koma ndikumbukila zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.

11 Ndidzakumbukila zimene adazicita Ambuye;Inde, ndidzakumbukila zodabwiza zanu zoyambira kale.

12 Ndipo ndidzalingalira nchito yanu yonse,Ndi kulingalirabe zimene munazicita Inu.

13 Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;Mulungu wamkuru ndani monga Mulungu?

14 Inu ndinu Mulungu wakucita codabwiza;Munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.

15 Munaombola anthu anu ndi mkonowanu,Ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.

16 Madziwo anakuonani Mulungu;Anakuonani madziwo; anacita mantha:Zozama zomwe zinanjenjemera,

17 Makongwa anatsanula madzi;Thambo lidamvetsa liu lace;Mibvi yanu yomwe inaturukira.

18 Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;Mphezi zinaunikira ponse pali anthu;Dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

19 Njira yanu inali m'nyanja,Koyenda Inu nku madzi akulu,Ndipo mapazi anu sanadziwika.

20 Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa,Ndi dzanja la Mose ndi Aroni,