1 Ndikweza maso anga kwa Inu,Kwa Inu wakukhala kumwamba.
2 Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye ao,Monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi:Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu,Kufikira aticitira cifundo.
3 Muticitire cifundo, Yehova, muticitire cifundo;Pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo.
4 Moyo wathu wakhuta ndithuNdi kuseka kwa iwo osasowa kanthu,Ndi mnyozo wa odzikuza.